1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Chiv. 20.8Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa kudziko la Magogi, ndiye mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; nunenere motsutsana naye,
3uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;
42Maf. 19.28ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'chibwano mwako ndi zokowera, ndi kukutulutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo ovala mokwanira onsewo, msonkhano waukulu ndi zikopa zotchinjiriza, onsewo ogwira bwino malupanga;
5Ezk. 27.10, 13Persiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi chikopa ndi chisoti chachitsulo;
6Gomeri ndi magulu ake onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ake onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.
7Ukonzekeretu, inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.
8Gen. 49.1Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.
9Yer. 4.13Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
10Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,
11nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzanka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;
12kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi chuma, okhala pakati padziko.
13Ezk. 27.12-22Sheba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisisi, ndi misona yake yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? Wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kuchoka nazo siliva ndi golide, kuchoka nazo zoweta ndi chuma, kulanda zankhondo zambiri?
14Chifukwa chake nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israele, sudzachidziwa kodi?
15Ezk. 38.6Ndipo udzatuluka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukulu ndi nkhondo yaikulu;
16Eks. 14.4; Ezk. 38.9ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.
17Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?
18Ndipo kudzachitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israele, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m'mphuno mwanga.
19Hag. 2.6-7Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele;
20Hos. 4.3motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama zakuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.
21Ower. 7.22; 1Sam. 14.20Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake.
22Mas. 11.6Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulufure.
23Mas. 9.16Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.