MASALIMO 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa

1 Miy. 4.14-15; Mas. 26.4 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,

kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa,

kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2 Mas. 119.35, 47, 92, 97 Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake;

ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.

3 Yer. 17.8 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;

wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake,

tsamba lake lomwe losafota;

ndipo zonse azichita apindula nazo.

4 Yes. 17.13 Oipa satero ai;

koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo,

kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.

6 Nah. 1.7; 2Tim. 2.19 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;

koma mayendedwe a oipa adzatayika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help