1 Mas. 119.1 Wodala yense wakuopa Yehova,
wakuyenda m'njira zake.
2 Yes. 3.10 Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako;
wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
3 Mas. 52.8; Ezk. 19.10 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako;
ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
4Taonani, m'mwemo adzadalitsika
munthu wakuopa Yehova.
5Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni;
ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
6 Gen. 50.23 Inde, udzaona zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.