AKOLOSE 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Atsate kuyeramtima, ndi chikondano cha pa abale

1 Aro. 6.5; 8.34 Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.

2Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

3Agal. 2.20Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

4Yoh. 11.25Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.

5 Aro. 8.13; Agal. 5.24 Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

6Aef. 5.6chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

7zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo.

8Aef. 4.22Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:

9Aef. 4.22-25musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,

10Aro. 12.2ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;

111Ako. 12.13pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

12 Agal. 5.22 Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;

13Mrk. 11.25kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

14Yoh. 13.34koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

15Afi. 4.7Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

16Aef. 5.19Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

171Ako. 10.31Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.

Za banja la munthu

18 Tit. 2.5 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

191Pet. 3.7Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.

20Aef. 6.1Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

21Aef. 6.4Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

22Aef. 6.6-7; 1Tim. 6.1Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;

23Aef. 6.6-7; 1Tim. 6.1chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

241Ako. 7.22; Aef. 6.8podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

25Aro. 2.11Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help