1Dzamveni kuno, anthu inu nonse;
tcherani khutu, inu nonse amakono,
2awamba ndi omveka omwe,
achuma ndi aumphawi omwe.
3Pakamwa panga padzanena zanzeru;
ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.
4Ndidzatchera khutu kufanizo,
ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.
5Ndidzaoperanji masiku oipa,
pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?
6 Mas. 52.7; Mrk. 10.24 Iwo akutama kulemera kwao;
nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;
7kuombola mbale sangadzamuombole,
kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.
8Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali,
ndipo chilekeke nthawi zonse.
9Kuti akhale ndi moyo osafa,
osaona chivundi.
10 Mlal. 2.16 Pakuti aona anzeru amafa,
monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,
nasiyira ena chuma chao.
11 Gen. 4.17 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire,
ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo;
atchapo dzina lao padziko pao.
12 Mlal. 3.19 Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa,
afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.
13 Luk. 12.20 Njira yao ino ndiyo kupusa kwao,
koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao.
14 1Ako. 6.2 Aikidwa m'manda ngati nkhosa;
mbusa wao ndi imfa.
Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao;
ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda,
kuti pokhala pake padzasowa.
15 Mas. 78.4-6 Koma Mulungu adzaombola moyo wanga
kumphamvu ya manda.
Pakuti adzandilandira ine.
16Usaope polemezedwa munthu,
pochuluka ulemu wa nyumba yake;
17 Luk. 12.19, 21 pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse;
ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
18Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo,
ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.
19Adzamuka kumbadwo wa makolo ake;
sadzaona kuunika nthawi zonse.
20 Mas. 49.12 Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,
afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.