1Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;
pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.
2Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;
Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.
3 Mas. 57.1 Mundichitire chifundo, Ambuye;
pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.
4Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;
pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.
5 Yow. 2.13 Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,
ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
6Tcherani khutu pemphero langa, Yehova;
nimumvere mau a kupemba kwanga.
7 Mas. 50.15 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;
popeza mudzandivomereza.
8 Eks. 15.11 Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;
ndipo palibe ntchito zonga zanu.
9 Yes. 66.23; Chiv. 15.4 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye;
nadzalemekeza dzina lanu.
10 Deut. 6.4; Mrk. 12.29 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa;
Inu ndinu Mulungu, nokhanu.
11 Mas. 25.2, 5 Mundionetse njira yanu, Yehova;
ndidzayenda m'choonadi chanu,
muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
12Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga,
ndi mtima wanga wonse;
ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
13 Mas. 116.8 Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu;
ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
14Mulungu, odzikuza andiukira,
ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,
ndipo sanaike Inu pamaso pao.
15 Eks. 34.6; Neh. 9.17 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo,
wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
16 Mas. 25.16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo;
mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,
ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17Mundichitire chizindikiro choti chabwino;
kuti ondida achione, nachite manyazi,
popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.