1 Deut. 10.12 Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.
2Deut. 8.5Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, ndi mkono wake wotambasuka,
3ndi zizindikiro zake, ndi ntchito zake, adazichitira Farao mfumu ya Aejipito, ndi dziko lake lonse pakati pa Ejipito;
4Eks. 14.27-28ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;
5ndi chimene anakuchitirani m'chipululu, kufikira munadza kumalo kuno;
6Num. 16.1ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
7Koma maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita.
8Yos. 1.6-9Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene munkako kulilandira;
9ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
10Pakuti dziko limene munkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;
11koma dziko limene munkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;
12ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.
Za madalitso otsatira kumvera kwao13 Deut. 28.1, 12 Ndipo kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,
14ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.
15Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.
16Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza;
171Maf. 8.35ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.
18Deut. 6.8Chifukwa chake muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m'moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pamaso anu.
19Deut. 4.9-10Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.
20Deut. 6.9Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu;
21kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo lili pamwamba padziko.
22Deut. 6.17-19Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kummamatira;
23Yehova adzapirikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu.
24Yos. 1.3Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.
25Deut. 7.24Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.
Mdalitso ndi temberero26 Deut. 30.1, 15, 19 Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero;
27Deut. 28.2-14dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino;
28Deut. 28.15-45koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.
29 Yos. 8.33 Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene munkako kulilandira, munene mdalitso paphiri la Gerizimu, ndi temberero paphiri la Ebala.
30Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m'tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More?
31Pakuti mulinkuoloka Yordani kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzachilandira cholowa chanu, ndi kukhalamo.
32Potero samalirani kuchita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.