1 1Mbi. 11.10; 27.1-31 Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.
22Sam. 7.2; Mas. 132.3-5, 7Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.
32Sam. 7.5-14Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.
4Komatu Yehova Mulungu wa Israele anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israele kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israele yense;
5ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.
6Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.
71Mbi. 22.13Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kosatha, akalimbika kuchita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.
8Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza.
91Sam. 16.7; 2Mbi. 15.2; Mas. 139.2-3; 101.2; Yer. 9.24; Yoh. 17.3Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
10Hag. 2.4Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.
Davide apereka kwa Solomoni chifaniziro ndi mirimo ya Kachisi11 Eks. 25.40; 1Mbi. 28.19 Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;
12ndi chifaniziro cha zonse anali nazo mwa mzimu, cha mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi cha zipinda zonse pozungulirapo, cha zosungiramo chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi cha zosungiramo chuma za zinthu zopatulika;
13ndi cha magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi cha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi cha zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;
14cha golide woyesedwa kulemera kwake wa zipangizo zagolide, wa zipangizo zonse za ntchito ya mtundu uliwonse; cha siliva wa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwake, wa zipangizo za ntchito ya mitundumitundu;
15mwa kulemera kwakenso cha zoikaponyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikaponyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikaponyali chilichonse;
16ndi golide woyesedwa kulemera kwake wa magome a mkate woonekera, wa gome lililonse; ndi siliva wa magome asiliva,
17ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golide woona, ndi cha mitsuko yake yagolide, woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse;
18Eks. 25.18-22ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta wa akerubi agolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova.
191Mbi. 28.11-12Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.
20Deut. 31.7-8Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.
21Eks. 35.25-26; 36.1-2; 1Mbi. 24.26Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu ntchito iliyonse pali onse ofuna eni ake aluso, achite za utumiki uliwonse; akulu omwe ndi anthu onse adzachita monga umo udzanenamo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.