1Wopanduka afunafuna chifuniro chake,
nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;
koma kungovumbulutsa za m'mtima mwake.
3Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;
manyazi natsagana ndi chitonzo.
4Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;
kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5 Lev. 19.15 Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino,
ngakhale kuchitira chetera wolungama.
6Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;
ndipo m'kamwa mwake muputa kukwapulidwa.
7 Mas. 140.9 M'kamwa mwa wopusa mumuononga,
milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.
8Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka,
zotsikira m'kati mwa mimba.
9Wogwira ntchito mwaulesi
ndiye mbale wake wa wosakaza.
10 2Sam. 22.3; Mas. 18.2 Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba;
wolungama athamangiramo napulumuka.
11Chuma cha wolemera ndicho mzinda wake wolimba;
alingalira kuti ndicho khoma lalitali.
12Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;
koma chifatso chitsogolera ulemu.
13 Yoh. 7.51 Wobwezera mau asanamvetse apusa,
nadzichititsa manyazi.
14Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;
koma ndani angatukule mtima wosweka?
15Mtima wa wozindikira umaphunzira;
khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16 Gen. 32.20; 1Sam. 25.27 Mtulo wa munthu umtsegulira njira,
numfikitsa pamaso pa akulu.
17Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;
koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.
18Maere aletsa makangano,
nulekanitsa amphamvu.
19Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta,
kulanda mzinda wolimba nkosavuta;
makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwake;
iye nadzakhuta phindu la milomo yake.
21 Mat. 12.37 Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;
wolikonda adzadya zipatso zake.
22 Miy. 31.10-13 Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino;
Yehova amkomera mtima.
23 Yak. 2.3 Wosauka amadandaulira;
koma wolemera ayankha mwaukali.
24 Yoh. 11.5 Woyanjana ndi ambiri angodziononga;
koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.