1 Mac. 11.29; Agal. 2.10 Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.
2Mac. 20.7; Chiv. 1.10Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
32Ako. 8.19Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.
4Mac. 11.29; Agal. 2.10Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.
Za maulendo akudza, ndi malonje a Paulo5 Mac. 19.21 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya;
6Aro. 15.24ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.
7Yak. 4.15Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.
8Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.
9Mac. 14.27Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.
10 Mac. 19.22 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;
111Tim. 4.12chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.
121Ako. 3.5Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.
13 Aef. 6.10; Afi. 1.27; 1Ate. 5.6 Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.
141Ako. 14.1Zanu zonse zichitike m'chikondi.
15 1Ako. 1.16; 2Ako. 9.1 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),
16Aheb. 13.17kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito.
172Ako. 11.9Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.
18Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere.
19 Aro. 16.3-5 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao.
20Aro. 16.16Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.
21 Akol. 4.18 Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa.
22Agal. 1.8-9Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.
23Aro. 16.20Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi inu.
24Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.