1 Mas. 44.9 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;
mwakwiya; tibwezereni.
2 2Mbi. 7.14 Mwagwedeza dziko, mwaling'amba.
Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.
3 Yes. 51.17, 22 Mwaonetsa anthu anu zowawa,
mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.
4 Mas. 20.5 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,
aikweze chifukwa cha choonadi.
5 Mas. 108.6-13 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,
pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.
6 Amo. 4.2 Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera,
ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
7 Gen. 49.10 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;
ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga;
Yuda ndiye wolamulira wanga.
8 2Sam. 8.12, 14 Mowabu ndiye mkhate wanga;
pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga.
Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.
9Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga?
Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
10 Mas. 60.1 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya?
Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.
11 Mas. 118.8 Tithandizeni kunsautso;
kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.
12 1Mbi. 19.13 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima,
ndipo Iye adzapondereza otisautsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.