MASALIMO 34 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide alemekeza Yehova womlanditsa, nafulumiza ena amtameSalimo la Davide; muja anasintha makhalidwe ake pamaso pa Abimeleki, amene anampirikitsa, ndipo anachoka.

1 Aef. 5.20; 1Ate. 5.18 Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse;

kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

2 1Sam. 2.1 Moyo wanga udzatamanda Yehova;

ofatsa adzakumva nadzakondwera.

3 Luk. 1.46 Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova,

ndipo tikweze dzina lake pamodzi.

4 Mat. 7.7 Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera,

nandilanditsa m'mantha anga onse.

5Iwo anayang'ana Iye nasanguluka;

ndipo pankhope pao sipadzachita manyazi.

6 Mas. 3.4 Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva,

nampulumutsa m'masautso ake onse.

7 Dan. 6.22; 2Maf. 6.17 Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye,

nawalanditsa iwo.

8 1Pet. 2.3 Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;

wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9Opani Yehova, inu oyera mtima ake;

chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10 Deut. 4.29, 40 Misona ya mkango isowa nimva njala,

koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11 Mas. 32.8 Idzani ananu ndimvereni ine,

ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12Munthu wokhumba moyo ndani,

wokonda masiku, kuti aone zabwino?

13 Yak. 1.26; 3.2-10 Uletse lilime lako lisatchule zoipa,

ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

14 Yes. 1.16-17 Futuka pazoipa, nuchite zabwino,

funa mtendere ndi kuulondola.

15 Mas. 33.18 Maso a Yehova ali pa olungama mtima,

ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

16 Yer. 44.11 Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa,

kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.

17Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva,

nawalanditsa kumasautso ao onse.

18 Mas. 51.17 Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka,

apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

19 2Tim. 3.11-12 Masautso a wolungama mtima achuluka,

koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

20Iye asunga mafupa ake onse;

silinathyoke limodzi lonse.

21 Mas. 94.23 Mphulupulu idzamupha woipa;

ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

22 2Sam. 4.9 Yehova aombola moyo wa anyamata ake,

ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help