1 Chiv. 5.6; 7.3-4 Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.
2Chiv. 1.15Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;
3Chiv. 14.1; 15.3ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.
42Ako. 11.2; Yak. 1.18; Chiv. 17.14Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.
5Zef. 3.13; Aef. 5.27Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwe bodza; ali opanda chilema.
Angelo atatu akulalikiratu ziweruziro za Mulungu6 Aef. 3.9-11 Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;
7Chiv. 15.4ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
8 Yes. 21.9; Yer. 51.7 Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.
9 Chiv. 13.14-16 Ndipo anawatsata mngelo wina, wachitatu, nanena ndi mau aakulu, Ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena padzanja lake
10Yes. 51.17iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasakaniza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;
11Yes. 34.10ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera kunthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chilombocho ndi fano lake, ndi iye aliyense akalandira lemba la dzina lake.
12Chiv. 12.17; 13.10Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.
13 1Ate. 4.16; 2Ate. 1.7 Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.
Masika a dzinthu ndi a mphesa14 Ezk. 1.26; Chiv. 6.2 Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa Munthu, wakukhala naye korona wagolide pamutu pake, ndi m'dzanja lake chisenga chakuthwa.
15Mat. 13.39Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi, wofuula ndi mau aakulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.
16Ndipo Iye wokhala pamtambo anaponya chisenga chake padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.
17Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi ali mu Mwamba, nakhala nacho chisenga chakuthwa nayenso.
18Yow. 3.13; Chiv. 16.8Ndipo mngelo wina anatuluka paguwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau aakulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.
19Chiv. 19.15Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.
20Yes. 63.3; Aheb. 13.12Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.