1Ndikweza maso anga kumapiri:
Thandizo langa lidzera kuti?
2 Mas. 124.8 Thandizo langa lidzera kwa Yehova,
wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3 1Sam. 2.9; Yes. 27.3 Sadzalola phazi lako literereke:
Iye amene akusunga sadzaodzera.
4Taonani, wakusunga Israele
sadzaodzera kapena kugona.
5 Yes. 25.4 Yehova ndiye wakukusunga;
Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.
6 Yes. 49.10 Dzuwa silidzawamba usana,
mwezi sudzakupanda usiku.
7 Mas. 97.10 Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse;
adzasunga moyo wako.
8 Deut. 28.6 Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.