AHEBRI 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aheb. 8.3-4 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:

2Aheb. 4.15; 7.28akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko;

3Mac. 18.21ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo.

4Mat. 12.31-32; Aheb. 10.26, 29Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.

5Yoh. 8.54; Mas. 2.7Koteronso Khristu sanadzilemekeze yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye,

Mwana wanga ndi Iwe,

lero Ine ndakubala Iwe.

6 Mas. 11.4 Monga anenanso mwina,

Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse

monga mwa dongosolo la Melkizedeki.

7 Mat. 26.39, 42, 44, 53 Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,

8Afi. 2.8angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;

9Aheb. 2.10ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;

10Aheb. 5.6wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.

11 Yoh. 16.12 Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.

12Aheb. 6.1; 1Ako. 3.1-3Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.

131Ako. 3.1-3Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda.

141Ako. 2.14-15Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help