1Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa.
2Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga?
Chiyani mwana wa zowinda zanga?
3 Deut. 17.17; Neh. 13.26 Musapereke mphamvu yako kwa akazi,
ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.
4 Yes. 5.22-23; Hos. 4.11 Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo;
akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?
5Kuti angamwe, naiwale malamulo,
naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.
6Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali,
ndi vinyo kwa owawa mtima;
7amwe, naiwale umphawi wake,
osakumbukiranso vuto lake.
8 Lev. 19.15; Yes. 1.17 Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula,
ndi mlandu wa amasiye onse.
9 Lev. 19.15; Yes. 1.17 Tsegula pakamwa pako
nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.
10 Rut. 3.11 Mkazi wangwiro ndani angampeze?
Pakuti mtengo wake uposa ngale.
11Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira,
sadzasowa phindu.
12Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa,
masiku onse a moyo wake.
13Afuna ubweya ndi thonje,
nachita mofunitsa ndi manja ake.
14Akunga zombo za malonda;
nakatenga zakudya zake kutali.
15 Aro. 12.11 Aukanso kusanake,
napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito.
16Asinkhasinkha za munda, naugula;
naoka mipesa ndi zipatso za manja ake.
17Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu,
nalimbitsa mikono yake.
18Azindikira kuti malonda ake ampindulira;
nyali yake sizima usiku.
19Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake,
nafumbata mtengo wake.
20 Aef. 4.28; Aheb. 13.16 Aolowera chikhato chake osauka;
natambasulira aumphawi manja ake.
21Saopera banja lake chipale chofewa;
pakuti banja lake lonse livala mlangali.
22 Chiv. 19.8, 14 Adzipangira zimbwi zamawangamawanga;
navala bafuta ndi guta wofiirira.
23 Miy. 12.4 Mwamuna wake adziwika kubwalo,
pokhala pakati pa akulu a dziko.
24Asoka malaya abafuta, nawagulitsa;
napereka mipango kwa ogulitsa malonda.
25Avala mphamvu ndi ulemu;
nangoseka nthawi ya m'tsogolo.
26Atsegula pakamwa pake ndi nzeru,
ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.
27Ayang'anira mayendedwe a banja lake,
sadya zakudya za ulesi.
28Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala;
mwamuna wake namtama, nati,
29Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro,
koma iwe uposa onsewo.
30Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe;
koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.
31Mumpatse zipatso za manja ake;
ndi ntchito zake zimtame kubwalo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.