MIYAMBO 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zochitira miyambo

1 1Maf. 4.32; Mlal. 12.9 Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele.

2Kudziwa nzeru ndi mwambo;

kuzindikira mau ozindikiritsa;

3kulandira mwambo wakusamalira machitidwe,

chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika;

4kuchenjeza achibwana,

kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;

5 Miy. 9.9 kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;

ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;

6kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake,

mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.

Munthu asalole oipa amchete

7 Miy. 9.10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa;

opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

8 Aef. 6.1, 2 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,

ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;

9pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako,

ndi mkanda pakhosi pako.

10 Gen. 39.7-8 Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.

11 Yes. 5.26 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,

tilalire osachimwa opanda chifukwa;

12tiwameze ali ndi moyo ngati manda,

ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake,

tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

14udzachita nafe maere,

tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi.

15 Mas. 1.1 Mwananga, usayende nao m'njira;

letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16 Yes. 59.7 pakuti mapazi ao athamangira zoipa,

afulumira kukhetsa mwazi.

17Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe;

18ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao.

19 1Tim. 6.10 Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere;

chilanda moyo wa eni ake.

Chenjezo la Nzeru

20Nzeru ifuula panja;

imveketsa mau ake pabwalo;

21iitana posonkhana anthu polowera pachipata;

m'mzinda inena mau ake,

22Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu?

Onyoza ndi kukonda kunyoza,

opusa ndi kuda nzeru?

23 Yow. 2.28 Tembenukani pamene ndikudzudzulani;

taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,

ndikudziwitsani mau anga.

24 Yes. 66.4 Chifukwa ndaitana, ndipo munakana;

ndatambasula dzanja langa,

ndipo panalibe analabadira;

25 Luk. 7.30 koma munapeputsa uphungu wanga wonse,

ndi kukana kudzudzula kwanga.

26 Mas. 2.4 Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu,

ndidzatonyola pakudza mantha anu;

27pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,

ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu;

pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.

28 Yer. 11.11; Yak. 4.3 Pamenepo adzandiitana,

koma sindidzavomera;

adzandifunatu, osandipeza ai;

29 Mas. 119.173 chifukwa anada nzeru,

sanafune kuopa Yehova;

30anakana uphungu wanga,

nanyoza kudzudzula kwanga konse;

31 Yes. 3.11; Agal. 6.7 momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,

nadzakhuta zolingalira zao.

32Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha;

ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.

33 Mas. 25.12-13 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,

nadzakhala phee osaopa zoipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help