1 Aef. 6.18-19 Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;
2Aro. 15.31ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro.
31Ako. 1.9Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
4Agal. 5.10koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.
51Mbi. 29.18Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu.
6 Aro. 16.17 Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
71Ako. 4.16; 1Ate. 2.10Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhale dwakedwake mwa inu;
8Mac. 18.3kapena sitinadye mkate chabe padzanja la munthu aliyense, komatu m'chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;
92Ate. 3.7; 1Ako. 9.6si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.
10Gen. 3.19; 1Ate. 4.11Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.
11Gen. 3.19; 1Ate. 4.11; 2Ate. 3.6Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina.
12Aef. 4.28Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.
13Agal. 6.9Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.
14Mat. 18.17Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.
151Ate. 5.14Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire ngati mbale.
16 Aro. 15.33 Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 1Ako. 16.21 Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga.
18Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.