2 AKORINTO 10 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ulamuliro wa Paulo mtumwi

1 2Ako. 12.5, 7, 9 Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;

22Ako. 13.2, 10koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.

3Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi,

4Aef. 6.13(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);

51Ako. 1.19ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;

62Ako. 7.15ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.

7Yoh. 7.24Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.

82Ako. 13.10Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;

9kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa makalatawo.

102Ako. 12.5, 7, 9Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.

11Yer. 9.24Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa makalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo.

12Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.

13Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

141Ako. 9.1Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikire kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Khristu:

15Aro. 15.20osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,

16kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale.

17Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;

18Aro. 2.29pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help