MIYAMBO 8 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nzeru ipambana m'kuchita kwake

1 Miy. 1.20-21 Kodi nzeru siitana,

luntha ndi kukweza mau ake?

2Iima pamwamba pa mtunda,

pa mphambano za makwalala;

3pambali pa chipata polowera m'mudzi,

polowa anthu pa makomo ifuula:

4Ndinu ndikuitanani, amuna,

mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.

5Achibwana inu, chenjerani,

opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;

6imvani, pakuti ndikanena zoposa,

ndi zolungama potsegula pakamwa panga.

7Pakuti m'kamwa mwanga mudzalankhula ntheradi,

zoipa zinyansa milomo yanga.

8Mau onse a m'kamwa mwanga alungama;

mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.

9Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;

alungama kwa akupeza nzeru.

10Landirani mwambo wanga, si siliva ai;

ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika.

11 Mas. 19.10 Pakuti nzeru iposa ngale,

ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo.

12Ine Nzeru ndikhala m'kuchenjera, ngati m'nyumba yanga;

ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.

13 Miy. 16.6 Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;

kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa,

ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

14Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;

ndine luntha; ndili ndi mphamvu.

15 Dan. 2.21; Aro. 13.1 Mwa ine mafumu alamulira;

akazembe naweruza molungama.

16Mwa ine akalonga ayang'anira,

ndi akulu, ngakhale oweruza onse a m'dziko.

17 1Sam. 2.30; Yoh. 14.21; Yak. 1.5 Akundikonda ndiwakonda;

akundifunafuna adzandipeza.

18 Mat. 6.33 Katundu ndi ulemu zili ndi ine,

chuma chosatha ndi chilungamo.

19Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka;

phindu langa liposa siliva wosankhika.

20Ndimayenda m'njira ya chilungamo,

pakati pa mayendedwe a chiweruzo,

21kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale cholowa chao,

ndi kudzaza mosungira mwao.

Nzeru ndiyo ya nthawi yosayamba

22Yehova anali nane poyamba njira yake,

asanalenge zake zakale.

23Anandiimika chikhalire chiyambire,

dziko lisanalengedwe.

24Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine,

pamene panalibe akasupe odzala madzi.

25Mapiri asanakhazikike,

zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa.

26Asanalenge dziko, ndi thengo,

ngakhale chiyambi cha fumbi la dziko.

27Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo;

pamene analemba pazozama kwetekwete;

28polimbitsa Iye thambo la kumwamba,

pokula akasupe a zozama.

29 Gen. 1.9, 10 Poikira nyanja malire ake,

kuti madzi asapitirire pa lamulo lake;

polemba maziko a dziko.

30Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri;

ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku,

ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;

31ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu,

ndi kusekerera ndi ana a anthu.

32Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,

ngodala akusunga njira zanga.

33Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.

34 Mas. 119.1-2; Luk. 11.28 Ngwodala amene andimvera,

nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku,

ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;

35pakuti wondipeza ine apeza moyo;

Yehova adzamkomera mtima.

36 Miy. 20.2 Koma wondichimwira apweteka moyo wake;

onse akundida ine akonda imfa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help