1Muimiranji patali, Yehova?
Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?
2 Mas. 7.16 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;
agwe m'chiwembu anapanganacho.
3 Mas. 94.4 Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake,
adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
4 Mas. 14.2 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira.
Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
5Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse;
maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;
adani ake onse awanyodola.
6Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine;
ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine.
7 Mas. 12.2 M'kamwa mwake mwadzala kutemberera
ndi manyengo ndi kuchenjerera;
pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
8 Mas. 17.11, 12 Akhala m'molalira midzi;
mobisalamo akupha munthu wosachimwa.
Ambisira waumphawi nkhope yake.
9Alalira monga mkango m'ngaka mwake;
alalira kugwira wozunzika,
agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
10Aunthama, nawerama,
ndipo aumphawi agwa m'zala zake.
11Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala;
wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.
12Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;
musaiwale ozunzika.
13Woipa anyozeranji Mulungu,
anena m'mtima mwake, Simudzafunsira?
14 Mas. 68.5; 2Tim. 1.12 Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso
ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu;
waumphawi adzipereka kwa Inu;
wamasiye mumakhala mthandizi wake.
15 Mas. 37.17 Thyolani mkono wa woipa;
ndipo wochimwa, mutsate choipa chake
kufikira simuchipezanso china.
16 Yer. 10.10 Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya;
aonongeka amitundu m'dziko lake.
17Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika,
mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;
18 Yes. 1.17 kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,
kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.