1 MAFUMU 21 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yezebele aphetsa Naboti

1Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wampesa, unali mu Yezireelemo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya.

21Sam. 8.14Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.

3Lev. 25.23; Num. 36.7; Ezk. 46.18Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.

41Maf. 20.43Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.

5Koma Yezebele mkazi wake anadza kwa iye, nati kwa iye, Muchitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezireele, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwake; koma anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wampesa.

7Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.

8M'mwemo analemba makalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza makalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mzinda mwake, nakhala naye, Naboti.

9Ndipo analemba m'makalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10Eks. 22.28; Mac. 6.11ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.

11Ndipo anthu aja a mzinda wake, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mzinda mwake, anachita monga Yezebele anawatumizira, monga munalembedwa m'makalata amene iye anawatumizira.

12Yes. 58.4Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

132Maf. 9.26Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mzinda, namponya miyala, namupha.

14Pomwepo anatuma mau kwa Yezebele, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15Ndipo kunali, atamva Yezebele kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebele anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wampesa wa Naboti Myezireele uja anakana kukugulitsani ndi ndalama, popeza Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti Myezireele wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wampesa wa Naboti, kuulandira.

Eliya auza Ahabu za kuonongeka kwa mbumba yake

17Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

18Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israele, akhala mu Samariya; taona, ali ku munda wampesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.

191Maf. 22.38Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.

201Maf. 18.17; 2Maf. 17.17; Aro. 7.14Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.

211Maf. 14.10; 2Maf. 9.8Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;

22ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.

232Maf. 9.33-36Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele.

241Maf. 14.11Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m'mzinda, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya.

251Maf. 16.30-33Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.

26Gen. 15.16; 2Maf. 21.11Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.

27Gen. 37.34Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a.

28Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

292Maf. 9.25Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help