MASALIMO 111 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Alemekeza Mulungu pa ntchito zao zazikulu zokoma

1 Mas. 35.18 Aleluya.

Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,

mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.

2 Mas. 143.5 Ntchito za Yehova nzazikulu,

zofunika ndi onse akukondwera nazo.

3Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu:

Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha.

4 Mas. 103.8 Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake;

Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.

5 Mat. 6.26, 33 Anapatsa akumuopa Iye chakudya;

adzakumbukira chipangano chake kosatha.

6Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake,

pakuwapatsa cholowa cha amitundu.

7 Mas. 19.9 Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo;

malangizo ake onse ndiwo okhulupirika.

8 Mat. 5.18 Achirikizika kunthawi za nthawi,

achitika m'choonadi ndi chilunjiko.

9 Mat. 1.21; Luk. 1.49 Anatumizira anthu ake chipulumutso;

analamulira chipangano chake kosatha;

dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.

10 Deut. 4.5-6; Miy. 1.7 Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru;

onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma;

chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help