MASALIMO 17 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide apempha Mulungu amsunge pa ofuna kumuonongaPemphero la Davide.

1Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga;

tcherani khutu ku pemphero langa

losatuluka m'milomo ya chinyengo.

2Pankhope panu patuluke chiweruzo changa;

maso anu apenyerere zolunjika.

3 Mas. 26.2; Zek. 13.9 Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;

mwandisuntha, simupeza kanthu;

mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.

4Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu

ndingalowe njira za woononga.

5 Mas. 44.18 M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu,

mapazi anga sanaterereke.

6 Mas. 116.2 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu;

tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.

7 Mas. 31.21 Onetsani chifundo chanu chodabwitsa,

Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu

kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.

8 Deut. 32.10; Mat. 23.37 Ndisungeni monga kamwana ka m'diso,

ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,

9kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,

adani a pa moyo wanga amene andizinga.

10Mafuta ao awatsekereza;

m'kamwa mwao alankhula modzikuza.

11Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu,

apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.

12Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,

ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.

13Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse,

landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;

14kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,

kwa anthu a dziko lapansi pano

amene cholowa chao chili m'moyo uno,

ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika;

akhuta mtima ndi ana,

nasiyira ana amakanda zochuluka zao.

15 Mas. 65.4; 1Yoh. 3.2 Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo,

ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help