NUMERI 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ntchito ya Alevi

1Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.

2Ndipo maina ao a ana aamuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

3Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe.

4Lev. 10.1Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.

5Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

6Sendera nalo kuno fuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.

7Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi.

8Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi.

9Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.

10Aro. 12.7Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.

11Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

12Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.

13Eks. 13.12; Luk. 2.23Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.

14Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, nati

15Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.

16Ndipo Mose anawawerenga monga mwa mau a Yehova, monga adamuuza.

17Ndipo ana a Levi maina ao ndi awa: Geresoni, ndi Kohati ndi Merari.

18Ndi ana a Geresoni maina ao ndi awa, monga mwa mabanja ao: Libini, ndi Simei.

19Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amuramu ndi Izihara, Hebroni ndi Uziyele.

20Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.

21Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Geresoni; ndiwo mabanja a Geresoni.

22Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.

23Mabanja a Ageresoni azimanga mahema ao pambuyo pa chihema kumadzulo.

24Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo a Ageresoni ndiye Eliyasafu mwana wa Laele.

25Ndipo udikiro wa ana a Geresoni m'chihema, chokomanako ndiwo Kachisi, ndi chihema, chophimba chake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako,

26ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.

27Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.

28Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pamalo opatulika.

29Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumwera.

30Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.

31Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.

32Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.

33Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo Amerari; ndiwo mabanja a Merari.

34Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi kudza mazana awiri.

35Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto.

36Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a chihema, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse;

37ndi nsichi za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake.

38Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.

39Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

40Ndipo Yehova anati kwa Mose, Werenga amuna oyamba kubadwa onse a ana a Israele kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu nuone chiwerengo cha maina ao.

41Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele.

42Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele.

43Ndipo amuna onse oyamba kubadwa, powerenga maina, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu atatu.

44Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

45Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.

46Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israele, akuposa Alevi, akaomboledwe,

47ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);

48nupereke ndalama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna.

49Pamenepo Mose analandira ndalama zoombola nazo kwa iwo akuposa aja adawaombola Alevi;

50analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

51Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help