MASALIMO 39 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kupepuka kwa moyo unoKwa Mkulu wa Nyimbo, kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

1 Mas. 141.3; Yak. 3.2 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,

kuti ndingachimwe ndi lilime langa.

Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa,

pokhala woipa ali pamaso panga.

2Ndinatonthola osanena mau,

ndinakhala chete osalawa chokoma;

ndipo chisoni changa chinabuka.

3Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine;

unayaka moto pakulingirira ine.

Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa,

4 Mas. 90.12 Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa,

ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;

ndidziwe malekezero anga.

5 Mas. 90.4 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;

ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu,

Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.

6 Luk. 12.20-21 Indedi munthu ayenda ngati mthunzi;

Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma,

ndipo sadziwa adzachilandira ndani?

7Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani?

Chiyembekezo changa chili pa Inu.

8Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse,

musandiike ndikhale chotonza cha wopusa.

9 2Sam. 16.10; Yob. 2.10 Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga;

chifukwa inu mudachichita.

10Mundichotsere chovutitsa chanu;

pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu.

11 Yes. 50.9 Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu,

mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete.

Indedi, munthu aliyense ali chabe.

12 2Mbi. 29.15; 2Ako. 5.6; Aheb. 11.13 Imvani pemphero langa, Yehova,

ndipo tcherani khutu kulira kwanga;

musakhale chete pa misozi yanga;

Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu,

wosakhazikika, monga makolo anga onse.

13 Yob. 10.20-21 Ndiloleni, kuti nditsitsimuke,

ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help