MIYAMBO 24 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mas. 37.1 Usachitire nsanje anthu oipa,

ngakhale kufuna kukhala nao;

2 Mas. 10.7 pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko;

milomo yao ilankhula za mphulupulu.

3Nzeru imangitsa nyumba;

luntha liikhazikitsa.

4Kudziwa kudzaza zipinda zake

ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.

5 Mlal. 9.16 Mwamuna wanzeru ngwamphamvu;

munthu wodziwa ankabe nalimba.

6 Miy. 20.18 Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo,

ndi kupulumuka pochuluka aphungu.

7Nzeru italikira chitsiru;

satsegula pakamwa kubwalo.

8Wolingalira zakuchita zoipa

anthu adzamtcha wachiwembu.

9Maganizo opusa ndiwo tchimo;

wonyoza anyansa anthu.

10Ukalefuka tsiku la tsoka

mphamvu yako ichepa.

11 Yes. 58.6-7; 1Yoh. 3.16 Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse;

omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.

12 Mas. 62.12; Yer. 32.19; Aro. 2.6 Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi;

kodi woyesa mitima sachizindikira ichi?

Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa?

Ndipo kodi sabwezera munthu yense

monga mwa machitidwe ake?

13Mwananga, idya uchi pakuti ngwabwino,

ndi chisa chake chitsekemera m'kamwa mwako.

14Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako;

ngati waipeza padzakhala mphotho,

ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.

15Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama;

usapasule popuma iyepo.

16 Est. 7.10; Mas. 34.19; Mik. 7.8 Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso;

koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.

17 Oba. 1.12 Usakondwere pakugwa mdani wako;

mtima wako usasekere pokhumudwa iye;

18kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa,

ndi kuleka kumkwiyira.

19 Mas. 37.1 Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa;

ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu.

20 Mas. 11.6 Pakuti woipayo sadzalandira mphotho;

nyali ya amphulupulu idzazima.

21 Aro. 13 Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe,

osadudukira anthu osinthasintha.

22Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka;

ndipo ndani adziwa chionongeko cha zaka zao?

23 Lev. 19.15; Yoh. 7.24 Izinso zili za anzeru,

poweruza chetera silili labwino.

24 Yes. 5.23 Wonena kwa woipa, Wolungama iwe;

magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira.

25Omwe amdzudzula adzasekera,

nadzadalitsika ndithu.

26Wobwezera mau oongoka

apsompsona milomo.

27Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda;

pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.

28 Aef. 4.25 Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa;

kodi udzanyenga ndi milomo yako?

29 Miy. 20.22 Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine

ndidzabwereza munthuyo monga mwa machitidwe ake.

30Ndinapita pamunda wa waulesi,

polima mphesa munthu wosowa nzeru.

31Taonani, ponsepo panamera minga,

ndi kuwirirapo khwisa;

tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.

32Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira,

ndinaona ndi kulandira mwambo.

33 Miy. 6.9-11 Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono,

kungomanga manja pang'ono m'kugona,

34ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala;

ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help