1 Ezk. 26—28 Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo.
2Khalani chete, inu okhala m'chisumbu; iwe amene anakudzazanso amalonda a ku Sidoni, opita m'nyanja.
3Ndi pa nyanja zazikulu anapindula ndi mbeu za ku Sihori ndizo dzinthu za ku mtsinje; ndi kumeneko kunali msika wa amitundu.
4Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.
5Yes. 19.16Pofika mbiriyo ku Ejipito, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Tiro.
6Olokani inu, kunka ku Tarisisi, kuwani, inu okhala m'chisumbu.
7Kodi umene ndi mzinda wanu wokondwa, wachikhalire kale lomwe, umene mapazi ake anaunyamula kunka nao kutali kukhalako?
8Ndani wapanga uphungu uno pa Tiro, mudzi umene upereka akorona, amalonda ake ali akalonga, ogulitsa ake ali olemekezeka padziko lapansi?
9Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.
10Pita pakati padziko lako monga mtsinje, iwe mwana wamkazi wa Tarisisi; palibenso lamba.
11Iye watambasula dzanja lake panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira Kanani za amalonda, kupasula malinga ake.
12Chiv. 18.22Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wovutidwa, mwanawamkazi wa Sidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.
13Mas. 72.9, 10Taonani, dziko la Ababiloni; anthu awa sakhalanso; Asiriya analiika ilo likhale la zilombo zokhala m'chipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ake; nalipasula.
14Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; pakuti linga lanu lapasulidwa.
15Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Tiro adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, chidzakhala kwa Tiro monga m'nyimbo ya mkazi wadama.
16Tenga mngoli, yendayenda m'mzinda, iwe mkazi wadama, amene unaiwalika; imba zokoma, chulukitsa nyimbo, kuti ukumbukiridwe.
17Chiv. 17.2Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Tiro, ndipo iye adzabwerera kumphotho yake, nadzachita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.
18Zek. 14.20, 21Malonda ake ndi mphotho yake zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; chifukwa malonda ake adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, navale chaulemu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.