AFILIPI 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Awachenjeza asatsate atumwi onyenga. Aonetsere zipatso za Mzimu

1 1Ate. 5.16 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

2Agal. 5.15Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula;

3Yoh. 4.23-24pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;

42Ako. 11.18, 21ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;

5Gen. 17.12; 2Ako. 11.22wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

6Mac. 9.1; Aro. 10.5monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine.

7Mat. 13.44Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu.

8Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,

9Aro. 3.21-22ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

10Aro. 6.3-5kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;

11ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.

121Tim. 6.12Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.

13Luk. 9.62; 1Ako. 9.24, 26Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

142Tim. 4.7-8ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

151Ako. 14.20Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;

16Agal. 6.15-16chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.

17 1Ako. 4.16 Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.

18Agal. 6.12Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;

192Ako. 11.15; Aro. 8.5; 16.18chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.

20Mac. 1.11; Akol. 3.1, 3Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;

211Ako. 15.43, 48-49amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help