1 Mas. 128.1 Odala angwiro m'mayendedwe ao,
akuyenda m'chilamulo cha Yehova.
2Odala iwo akusunga mboni zake,
akumfuna ndi mtima wonse;
3 Yoh. 3.9; 5.18 inde, sachita chosalungama;
ayenda m'njira zake.
4Inu munatilamulira,
tisamalire malangizo anu ndi changu.
5Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga
kuti ndisamalire malemba anu.
6 1Yoh. 2.28 Pamenepo sindidzachita manyazi,
pakupenyerera malamulo anu onse.
7Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka,
pakuphunzira maweruzo anu olungama.
8Ndidzasamalira malemba anu:
Musandisiye ndithu.
9Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?
Akawasamalira monga mwa mau anu.
10 2Mbi. 15.15 Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;
ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.
11 Luk. 2.19, 51 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,
kuti ndisalakwire Inu.
12Inu ndinu wodala Yehova;
ndiphunzitseni malemba anu.
13Ndinafotokozera ndi milomo yanga
maweruzo onse a pakamwa panu.
14Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,
koposa ndi chuma chonse.
15 Mas. 1.2 Ndidzalingirira pa malangizo anu,
ndi kupenyerera mayendedwe anu.
16Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;
sindidzaiwala mau anu.
17 Mas. 116.7 Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;
ndipo ndidzasamalira mau anu.
18Munditsegulire maso, kuti ndipenye
zodabwitsa za m'chilamulo chanu.
19 Gen. 47.9 Ine ndine mlendo padziko lapansi;
musandibisire malamulo anu.
20 Mas. 42.1-2 Mtima wanga wasweka ndi kukhumba
maweruzo anu nyengo zonse.
21Munadzudzula odzikuza otembereredwa,
iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.
22Mundichotsere chotonza, ndi chimpepulo;
pakuti ndinasunga mboni zanu.
23 Mas. 119.15 Nduna zomwe zinakhala zondineneza;
koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.
24Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa,
ndizo zondipangira nzeru.
25 Mas. 44.25; 143.11 Moyo wanga umamatika ndi fumbi;
mundipatse moyo monga mwa mau anu.
26Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:
Mundiphunzitse malemba anu.
27 Mas. 119.15 Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;
kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.
28Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni:
Mundilimbitse monga mwa mau anu.
29Mundichotsere njira ya chinyengo;
nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu.
30Ndinasankha njira yokhulupirika;
ndinaika maweruzo anu pamaso panga.
31Ndimamatika nazo mboni zanu;
musandichititse manyazi, Yehova.
32 1Maf. 4.29; Yes. 60.5; 2Ako. 6.11, 13 Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,
mutakulitsa mtima wanga.
33 Mat. 10.22 Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;
ndidzaisunga kufikira kutha kwake.
34 Miy. 2.6; Yak. 1.5 Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;
ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
35Mundiyendetse mopita malamulo anu;
pakuti ndikondwera m'menemo.
36 Luk. 12.15 Lingitsani mtima wanga kumboni zanu,
si ku chisiriro ai.
37 Miy. 23.5 Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe,
mundipatse moyo mu njira yanu.
38 2Sam. 7.25 Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,
ndiye wodzipereka kukuopani.
39Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho;
popeza maweruzo anu ndi okoma.
40Taonani, ndinalira malangizo anu;
mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.
41 Mas. 106.4 Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova,
ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu.
42Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;
popeza ndikhulupirira mau anu.
43Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga;
pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalire
kunthawi za nthawi.
45Ndipo ndidzayenda mwaufulu;
popeza ndinafuna malangizo anu.
46 Mat. 10.18-19; Mac. 26.1-2 Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,
osachitapo manyazi.
47Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,
amene ndiwakonda.
48Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;
ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.
49Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu,
amene munandiyembekezetsa nao.
50 Aro. 15.4 Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi;
pakuti mau anu anandipatsa moyo.
51 Yer. 20.7 Odzikuza anandinyoza kwambiri:
koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.
52Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,
ndipo ndinadzitonthoza.
53 Ezr. 9.3 Ndinasumwa kwakukulu,
chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.
54Malemba anu anakhala nyimbo zanga
m'nyumba ya ulendo wanga.
55 Mas. 63.6 Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova,
ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.
56Ichi ndinali nacho,
popeza ndinasunga malangizo anu.
57 Mali. 3.24 Yehova ndiye gawo langa:
Ndinati ndidzasunga mau anu.
58Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:
Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.
59 Luk. 15.17-18 Ndinaganizira njira zanga,
ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.
60Ndinafulumira, osachedwa,
kusamalira malamulo anu.
61Anandikulunga nazo zingwe za oipa;
koma sindinaiwale chilamulo chanu.
62 Mac. 16.25 Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani
chifukwa cha maweruzo anu olungama.
63Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,
ndi iwo akusamalira malangizo anu.
64 Mas. 33.5 Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, Yehova;
mundiphunzitse malemba anu.
65Munachitira mtumiki wanu chokoma, Yehova,
monga mwa mau anu.
66Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru;
pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.
67 Yer. 31.18-19 Ndisanazunzidwe ndinasokera;
koma tsopano ndisamalira mau anu.
68 Mat. 19.17 Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino;
mundiphunzitse malemba anu.
69 Yob. 13.4 Odzikuza anandipangira bodza:
Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70 Mac. 28.27 Mtima wao unona ngati mafuta;
koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.
71 Aheb. 12.10-11 Kundikomera kuti ndinazunzidwa;
kuti ndiphunzire malemba anu.
72 Miy. 8.10-11, 19 Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera
koposa golide ndi siliva zikwizikwi.
73 Mas. 100.3 Manja anu anandilenga nandiumba;
mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.
74 Mas. 34.2 Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;
popeza ndayembekezera mau anu.
75 Aheb. 12.10 Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,
ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.
76Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani,
monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.
77Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo;
popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.
78 Mas. 25.3 Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza:
Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
79Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,
ndipo adzadziwa mboni zanu.
80Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu;
kuti ndisachite manyazi.
81 Mas. 84.2 Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu:
Ndinayembekezera mau anu.
82 Mas. 69.3 Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,
ndikuti, Mudzanditonthoza liti?
83Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;
koma sindiiwala malemba anu.
84 Chiv. 6.10 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?
Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?
85Odzikuza anandikumbira mbuna,
ndiwo osasamalira chilamulo chanu.
86Malamulo anu onse ngokhulupirika;
andilondola nalo bodza; ndithandizeni.
87Akadandithera padziko lapansi;
koma ine sindinasiye malangizo anu.
88Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu;
ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.
89 Mat. 24.34-35 Mau anu aikika kumwamba,
kosatha, Yehova.
90Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo;
munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.
91Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero;
pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.
92Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa,
ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.
93Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;
popeza munandipatsa nao moyo.
94Ine ndine wanu, ndipulumutseni
pakuti ndinafuna malangizo anu.
95Oipa anandilalira kundiononga;
koma ndizindikira mboni zanu.
96Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse;
koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.
97 Mas. 1.2 Ha! Ndikondadi chilamulo chanu;
ndilingiriramo ine tsiku lonse.
98 Deut. 4.6, 8 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;
pakuti akhala nane chikhalire.
99Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;
pakuti ndilingalira mboni zanu.
100 Yob. 32.7-9 Ndizindikira koposa okalamba
popeza ndinasunga malangizo anu.
101 Miy. 1.15-16 Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa,
kuti ndisamalire mau anu.
102Sindinapatukane nao maweruzo anu;
pakuti Inu munandiphunzitsa.
103 Mas. 19.10 Mau anu azunadi powalawa ine!
Koposa uchi m'kamwa mwanga.
104Malangizo anu andizindikiritsa;
chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.
105 Miy. 6.23 Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,
ndi kuunika kwa panjira panga.
106 Neh. 10.29 Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,
kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.
107Ndazunzika kwambiri:
Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.
108 Aheb. 13.15 Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,
ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
109Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire;
koma sindiiwala chilamulo chanu.
110 Mas. 140.5 Oipa ananditchera msampha;
koma sindinasokere m'malangizo anu.
111 Deut. 33.4 Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha;
pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu,
kosatha, kufikira chimaliziro.
113 Yak. 1.8 Ndidana nao a mitima iwiri;
koma ndikonda chilamulo chanu.
114 Mas. 32.7 Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa;
ndiyembekezera mau anu.
115 Mas. 6.8 Mundichokere ochita zoipa inu;
kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116 Aro. 5.5; 9.33; 10.11 Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;
ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa.
117Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,
ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire.
118Mupepula onse akusokera m'malemba anu;
popeza chinyengo chao ndi bodza.
119Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala:
Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.
120 Hab. 3.16 Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;
ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.
121Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo;
musandisiyira akundisautsa.
122 Aheb. 7.22 Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere;
odzikuza asandisautse.
123Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu,
ndi mau a chilungamo chanu.
124Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu,
ndipo ndiphunzitseni malemba anu.
125 Mas. 116.16 Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;
kuti ndidziwe mboni zanu.
126Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu;
pakuti anaswa chilamulo chanu.
127 Mas. 119.72 Chifukwa chake ndikonda malamulo anu
koposa golide, inde golide woyengeka.
128Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika
malangizo anu onse akunena zonse;
koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
129Mboni zanu nzodabwitsa;
chifukwa chake moyo wanga uzisunga.
130 Miy. 1.4 Potsegulira mau anu paunikira;
kuzindikiritsa opusa.
131Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu;
popeza ndinakhumba malamulo anu.
132Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo,
monga mumatero nao akukonda dzina lanu.
133 Aro. 6.12 Khazikitsani mapazi anga m'mau anu;
ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.
134 Luk. 1.74 Mundiombole kunsautso ya munthu:
Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.
135 Mas. 4.6 Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;
ndipo mundiphunzitse malemba anu.
136 Yer. 14.17 Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi,
popeza sasamalira chilamulo chanu.
137 Ezr. 9.15 Inu ndinu wolungama, Yehova,
ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.
138 Mas. 19.7-9 Mboni zanuzo mudazilamulira
zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.
139 Mas. 69.9 Changu changa chinandithera,
popeza akundisautsa anaiwala mau anu.
140 Miy. 30.5 Mau anu ngoyera ndithu;
ndi mtumiki wanu awakonda.
141Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;
koma sindiiwala malemba anu.
142 Yoh. 17.17 Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha;
ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.
143Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;
koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
144Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;
mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.
145Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;
ndidzasunga malemba anu.
146Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,
ndipo ndidzasamalira mboni zanu.
147 Mas. 130.6 Ndinafuula kusanake:
ndinayembekezera mau anu.
148 Mas. 63.1, 6 Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku,
kuti ndilingirire mau anu.
149Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu;
mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.
150Otsata zachiwembu andiyandikira;
akhala kutali ndi chilamulo chanu.
151 Mas. 145.18 Inu muli pafupi, Yehova;
ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.
152 Luk. 21.33 Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,
kuti munazikhazika kosatha.
153 Mali. 5.1 Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;
pakuti sindiiwala chilamulo chanu.
154 1Sam. 24.15 Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;
mundipatse moyo monga mwa mau anu.
155 Yob. 5.4 Chipulumutso chitalikira oipa;
popeza safuna malemba anu.
156Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova;
mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.
157 Mas. 44.18 Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri;
koma sindinapatukane nazo mboni zanu.
158 Ezk. 9.4 Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;
popeza sasamalira mau anu.
159Penyani kuti ndikonda malangizo anu;
mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu.
160Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi;
ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161 1Sam. 24.11, 14 Nduna zinandilondola kopanda chifukwa;
koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu.
162Ndikondwera nao mau anu,
ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.
163Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;
koma ndikonda chilamulo chanu.
164Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,
chifukwa cha maweruzo anu olungama.
165 Yes. 32.17 Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri;
ndipo alibe chokhumudwitsa.
166 Gen. 49.18 Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova,
ndipo ndinachita malamulo anu.
167Moyo wanga unasamalira mboni zanu;
ndipo ndizikonda kwambiri.
168 Miy. 5.21 Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;
popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.
169Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova;
mundizindikiritse monga mwa mau anu.
170Kupemba kwanga kudze pamaso panu;
mundilanditse monga mwa mau anu.
171 Mas. 119.7 Milomo yanga itulutse chilemekezo;
popeza mundiphunzitsa malemba anu.
172Lilime langa liimbire mau anu;
pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.
173 Yos. 24.22; Luk. 10.42 Dzanja lanu likhale lakundithandiza;
popeza ndinasankha malangizo anu.
174Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova;
ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.
175Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;
ndipo maweruzo anu andithandize.
176 Yes. 53.6; Luk. 15.4; 1Pet. 2.25 Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu;
pakuti sindiiwala malamulo anu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.