1 Luk. 12.19-20 Usanyadire zamawa,
popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?
2 2Ako. 10.12, 18 Wina akutume, si m'kamwa mwako ai;
mlendo, si milomo ya iwe wekha.
3Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu;
koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.
4 1Yoh. 3.12 Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka;
koma ndani angalakike ndi nsanje?
5 Agal. 2.14 Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.
6 Mas. 141.5; Mat. 26.49 Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika;
koma mdani apsompsona kawirikawiri.
7Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi;
koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.
8Monga mbalame yosochera kuchisa chake,
momwemo munthu wosochera kumalo ake.
9Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima,
ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
10Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye;
usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako;
mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
11Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga;
kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.
12Wochenjera aona zoipa, nabisala;
koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.
13Tenga malaya a woperekera mlendo chikole;
woperekera mkazi wachiwerewere chikole umgwire mwini.
14Yemwe adalitsa mnzake ndi mau aakulu pouka mamawa,
anthu adzachiyesa chimenecho temberero.
15 Miy. 19.13 Kudonthadontha tsiku lamvula,
ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.
16Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo;
dzanja lake lamanja lingogwira mafuta.
17Chitsulo chinola chitsulo;
chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.
18 1Ako. 9.7, 13 Wosunga mkuyu adzadya zipatso zake;
wosamalira ambuyake adzalemekezedwa.
19Monga m'madzi nkhope zionana,
momwemo mitima ya anthu idziwana.
20 Mlal. 1.8 Kunsi kwa manda ndi kuchionongeko sikukhuta;
ngakhale maso a munthu sakhutai.
21 Siliva asungunuka m'mbiya,
ndi golide m'ng'anjo,
motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.
22 Yer. 5.3 Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale,
koma utsiru wake sudzamchoka.
23Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji,
samalira magulu ako;
24pakuti chuma sichili chosatha;
kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.
25Amatuta udzu, msipu uoneka,
atchera masamba a kumapiri.
26Anaankhosa akuveka,
atonde aombolera munda;
27mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya;
ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.