ESTERE Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaBukuli likukamba za Estere, mtsikana wina wachiyuda, amene ankakonda kwambiri anthu a mtundu wake, naonetsa kulimba mtima kwake pothandiza kuwapulumutsa Ayudawo kwa adani ao. Lifotokozanso za chiyambi chake komanso tanthauzo la chikondwerero cha Chiyuda chotchedwa Purimu.Za mkatimuEstere asankhidwa kuti akhale mfumukazi kudziko la Persiya 1.1—2.23 Hamani apanga chiwembu chofuna kuwonongeratu fuko la Ayuda 3.1—5.14Hamani atsutsidwa naphedwa 6.1—7.10Ayuda agonjetsa adani ao 8.1—10.3