1Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkulu Estere.
2Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.
3Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;
4Est. 3.9, 13pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadatha kubwezera kusowa kwa mfumu.
5Pamenepo mfumu Ahasuwero inalankhula, niti kwa mkazi wamkulu Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wake kuti azitero?
6Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkulu.
7Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.
8Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m'nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.
9Est. 5.14; Mas. 7.16Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.
10Mas. 37.35-36; Dan. 6.24Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.