1Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete, ndi chifukwa cha Yerusalemu sindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka.
2Yes. 60.3; Chiv. 14.19-20Ndipo amitundu adzaona chilungamo chako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzatchedwa dzina latsopano, limene m'kamwa mwa Yehova mudzatchula.
3Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wachifumu m'dzanja la Mulungu wako.
41Pet. 2.10Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.
5Yes. 65.19Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.
6 Ezk. 3.17 Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,
7ndipo musamlole akhale chete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi.
8Deut. 28.31Yehova analumbira padzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;
9koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.
10 Yes. 11.12; 40.3 Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; chotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.
11Zek. 9.9; Mat. 21.5Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.
12Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mzinda wosasiyidwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.