YOBU 40 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,

2Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?

Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.

3Pamenepo Yobu anayankha Yehova nati,

4 Ezr. 9.6; Mas. 39.9; 51.4 Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?

Ndigwira pakamwa.

5Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;

inde kawiri, koma sindionjezanso.

6Ndipo Yehova anamyankha Yobu m'kamvulumvulu, nati,

7Dzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna;

ndidzakufunsa, undidziwitse.

8 Aro. 3.4 Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi?

Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi,

kuti ukhale wolungama ndiwe?

9 Mas. 29.3, 4 Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?

Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

10Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,

nuvale ulemu ndi ulemerero.

11Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,

nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa.

12 Dan. 4.37 Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse,

nupondereze oipa pomwe akhala.

13Uwakwirire pamodzi m'fumbi,

uzimange nkhope zao pobisika.

14Pamenepo inenso ndidzakuvomereza,

kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa.

15Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,

ikudya udzu ngati ng'ombe.

16Tapenya tsono, mphamvu yake ili m'chuuno mwake,

ndi kulimbalimba kwake kuli m'mitsempha ya m'mimba yake.

17Igwedeza mchira wake ngati mkungudza;

mitsempha ya ntchafu zake ipotana.

18Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa;

ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.

19Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu;

wakuilenga anaininkha lupanga lake.

20 Mas. 104.14 Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya,

kumene zisewera nyama zonse zakuthengo.

21Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,

pobisala pabango ndi pathawale.

22Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,

misondodzi ya kumtsinje iizinga.

23Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;

ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake.

24Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi?

Kapena kuboola m'mphuno mwake ili m'khwekhwe?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help