YESAYA 30 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Tsoka okhulupirira Ejipito

1 Deut. 29.19 Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;

2Yes. 31.1amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito!

3Yer. 37.5, 7Chifukwa chake mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito kudzakhala chisokonezo chanu.

4Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi.

5Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi chitonzo.

6Katundu wa zilombo za kumwera.

M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.

7Yes. 36.6Pakuti thangata la Ejipito lili lachabe, lopanda pake; chifukwa chake ndamutcha Wonyada, wokhala chabe.

8Hab. 2.2Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe kunthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.

9Deut. 32.20Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova;

101Maf. 22.13; Yer. 11.21amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;

11chokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu.

12Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo;

13Mas. 62.3chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.

14Yer. 19.11Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.

15Eks. 14.13-14; Yes. 30.7Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.

16Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; chifukwa chake inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; chifukwa chake iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.

17Lev. 26.8Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba paphiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.

18Mas. 34.8; Yer. 17.7Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

19Yes. 65.9Pakuti anthu adzakhala mu Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.

20Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;

21Yos. 1.7ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

22Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.

23Mat. 6.33; 1Tim. 4.8Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.

24Momwemonso ng'ombe ndi ana a bulu olima nthaka adzadya chakudya chochezera, chimene chapetedwa ndi chokokolera ndi mkupizo.

25Ndipo pamwamba pa mapiri aakulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa.

26Yes. 60.19-20Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa chilonda chimene anawakantha ena.

27Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi aakulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;

28ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m'nsagwada za anthu.

29Mas. 42.4Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.

30Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.

31Yes. 37.36Pakuti ndi mau a Yehova Aasiriya adzathyokathyoka, ndi ndodo yake adzammenya.

32Ndipo nthawi zonse Yehova adzawakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyanathunyana, Iye adzamenyana nao.

33Yer. 7.31Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help