1 1Sam. 26.20; Mas. 56.11 Ndakhulupirira Yehova,
mutani nkunena kwa moyo wanga,
Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
2Pakuti, onani, oipa akoka uta,
apiringidza muvi wao pansinga,
kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
3Akapasuka maziko,
wolungama angachitenji?
4 Mas. 33.13-14; Yes. 66.1; Hab. 2.20 Yehova ali mu Kachisi wake woyera,
Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba;
apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
5 Gen. 22.1; Yak. 1.12 Yehova ayesa wolungama mtima,
koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.
6 Ezk. 38.22 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa;
moto ndi miyala ya sulufure,
ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
7 Mas. 45.7; 1Yoh. 3.2 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama;
woongoka mtima adzapenya nkhope yake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.