EZEKIELE 9 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Malango a pa ochimwa

1Pamenepo Iye anafuula m'makutu mwanga ndi mau aakulu, ndi kuti, Asendere oyang'anira mzinda, aliyense ndi chida chake choonongera m'dzanja lake.

2Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m'dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.

3Ezk. 8.4Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pa kerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake.

4Eks. 12.7; 2Ako. 12.21; Chiv. 7.3Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.

5Nati kwa enawo, ndilikumva ine, Pitani pakati pa mzinda kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo;

62Mbi. 36.17; Chiv. 9.4iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.

7Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anatuluka, nakantha m'mzindamo.

8Yos. 7.6Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?

9Ezk. 8.12Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.

10Ezk. 8.18Ndipo Inenso diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yao pamutu pao.

11Ndipo taonani, munthu wovala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake, anabweza mau, ndi kuti, Ndachita monga munandilamulira ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help