MIYAMBO 26 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Monga chipale chofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika,

momwemo ulemu suyenera chitsiru.

2Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka,

momwemo temberero la pachabe silifikira.

3 Mas. 32.9 Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham'kamwa chiyenera bulu,

ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.

4Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake,

kuti ungafanane nacho iwe wekha.

5 Mat. 16.1-4; 21.24-27 Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake,

kuti asadziyese wanzeru.

6Wotumiza mau ndi dzanja la chitsiru

adula mapazi ake, namwa zompweteka.

7Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka,

momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

8Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala,

momwemo wochitira chitsiru ulemu.

9Monga munga wolasa dzanja la woledzera,

momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

10Monga woponya mivi ndi kulasa onse,

momwemo wolembera chitsiru,

ndi wolembera omwe alikupita panjira.

11 2Pet. 2.22; Eks. 8.15 Monga galu abweranso kumasanzi ake,

momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake.

12 Luk. 18.11; Aro. 12.10 Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru?

Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai.

13Waulesi ati, Mkango uli panjira,

wobangulawo uli m'makwalala.

14Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu,

momwemo waulesi agubuduka pakama pake.

15Waulesi alonga dzanja lake m'mbale;

kumtopetsa kulibweza kukamwa kwake.

16Waulesi adziyesa wanzeru

koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.

17Wakungopita ndi kuvutika ndi ndeu yosakhala yake

akunga wogwira makutu a galu.

18Monga woyaluka woponya nsakali,

mivi, ndi imfa,

19 Aef. 5.4 momwemo wonyenga mnzake ndi kuti,

ndi kusewera kumeneku.

20Posowa nkhuni moto ungozima;

ndi popanda kazitape makangano angoleka.

21Monga makala ozizira pa makala akunyeka,

ndi nkhuni pamoto;

momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.

22Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka

zitsikira m'kati mwa mimba.

23Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa

ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala ya siliva.

24Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake;

koma akundika chinyengo m'kati mwake.

25 Yer. 9.8 Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire;

pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.

26Angakhale abisa udani wake pochenjera,

koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.

27 Mas. 7.15-16; Mlal. 10.8 Wokumba dzenje adzagwamo,

wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.

28Lilime lonama lida omwewo linawasautsa;

ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help