MIYAMBO 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Wokonda mwambo akonda kudziwa;

koma wakuda chidzudzulo apulukira.

2Yehova akomera mtima munthu wabwino;

koma munthu wa ziwembu amtsutsa.

3Munthu sadzakhazikika ndi udyo,

muzu wa olungama sudzasunthidwa.

4 1Ako. 11.7 Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake;

koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.

5Maganizo a olungama ndi chiweruzo;

koma uphungu wa oipa unyenga.

6Mau a oipa abisalira mwazi;

koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.

7 Mat. 7.24-27 Oipa amagwa kuli zii;

koma banja la olungama limaimabe.

8 1Sam. 25.17 Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake;

koma wokhota mtima adzanyozedwa.

9Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo,

aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.

10 Deut. 25.4 Wolungama asamalira moyo wa choweta chake;

koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.

11 Gen. 3.19 Zakudya zikwanira wolima minda yake;

koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.

12Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu;

koma muzu wa olungama umabala zipatso.

13M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;

koma wolungama amatuluka m'mavuto.

14 Yes. 3.10-11 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake;

zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.

15 Luk. 18.11 Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake;

koma wanzeru amamvera uphungu.

16Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa;

koma wanzeru amabisa manyazi.

17Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo;

koma mboni yonama imanyenga.

18 Mas. 59.7 Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;

koma lilime la anzeru lilamitsa.

19 Mas. 52.4-5 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;

koma lilime lonama likhala kamphindi.

20Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa;

koma aphungu a mtendere amakondwa.

21Palibe vuto lidzagwera wolungama;

koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.

22 Chiv. 22.15 Milomo yonama inyansa Yehova;

koma ochita ntheradi amsekeretsa.

23Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;

koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.

24Dzanja la akhama lidzalamulira;

koma waulesi adzakhala ngati kapolo.

25 Yes. 50.4 Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;

koma mau abwino aukondweretsa.

26Wolungama atsogolera mnzake;

koma njira ya oipa iwasokeretsa.

27Waulesi samaotcha nyama yake anaigwira;

koma wolungama amalandira chuma chopambana cha anthu.

28M'khwalala la chilungamo muli moyo;

m'njira ya mayendedwe ake mulibe imfa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help