MASALIMO 81 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mulungu atonza Aisraele pa kusamvera kwaoKwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gititi. Salimo la Asafu.

1Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu;

fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo.

2Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka,

zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.

3Ombani lipenga, pokhala mwezi,

utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.

4 Num. 10.10 Pakuti ichi ndi cholemba cha kwa Israele,

chiweruzo cha Mulungu wa Yakobo.

5Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe,

pakutuluka iye kudziko la Ejipito.

Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

6 Yes. 9.4 Ndinamchotsera katundu paphewa pake,

manja ake anamasuka ku chotengera.

7 Eks. 2.23; 17.6-7; 19.16, 19 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;

ndinakuvomereza mobisalika m'bingu;

ndinakuyesa kumadzi a Meriba.

8Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni;

Israele, ukadzandimvera!

9 Eks. 20.3, 5; Yes. 43.12 Kwanu kusakhale mulungu wofuma kwina;

nusagwadire mulungu wachilendo.

10 Eks. 20.2; Yoh. 15.7; Aef. 3.20 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza

kukuchotsa kudziko la Ejipito;

yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.

11Koma anthu anga sanamvere mau anga;

ndipo Israele sanandivomere.

12 Mac. 7.42; 14.16 Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,

ayende monga mwa uphungu waowao.

13 Yes. 48.18 Ha! Akadandimvera anthu anga,

akadayenda m'njira zanga Israele!

14Ndikadagonjetsa adani ao msanga,

ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

15Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga,

koma nyengo yao ikadakhala yosatha.

16 Deut. 32.13-14 Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa,

ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help