MASALIMO 109 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide apempha Mulungu alange oipa, amlanditse m'manja mwaoKwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide.

1 Mas. 57.7-11; 83.1-2 Mulungu wa chilemekezo changa, musakhale chete;

2pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira;

anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.

3 Mas. 35.7; Yoh. 15.25 Ndipo anandizinga ndi mau a udani,

nalimbana nane kopanda chifukwa.

4M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani;

koma ine, kupemphera ndiko.

5Ndipo anandisenza choipa m'malo mwa chokoma,

ndi udani m'malo mwa chikondi changa.

6 Zek. 3.1 Muike munthu woipa akhale mkulu wake;

ndi mdani aime padzanja lamanja lake.

7Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika;

ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa.

8Masiku ake akhale owerengeka;

wina alandire udindo wake.

9 Eks. 22.22-24 Ana ake akhale amasiye,

ndi mkazi wake wamasiye.

10Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha;

afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao.

11Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;

ndi alendo alande za ntchito yake.

12Pasakhale munthu wakumchitira chifundo;

kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye.

13Zidzukulu zake zidulidwe;

dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.

14 Eks. 20.5 Mphulupulu za makolo ake zikumbukike ndi Yehova;

ndi tchimo la mai wake lisafafanizidwe.

15Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire,

kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi.

16Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo,

koma analondola wozunzika ndi waumphawi,

ndi wosweka mtima, kuti awaphe.

17 Miy. 14.14 Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini;

sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.

18Anavalanso temberero ngati malaya,

ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi,

ndi ngati mafuta m'mafupa ake.

19Limkhalire ngati chovala adzikuta nacho,

ndi lamba limene adzimangirira nalo m'chuuno chimangirire.

20Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova,

ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.

21Koma Inu, Yehova Ambuye,

muchite nane chifukwa cha dzina lanu;

ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.

22Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi,

ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga.

23Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali;

ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.

24Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala;

ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.

25 Mas. 22.6; Mat. 27.39 Ndiwakhaliranso chotonza;

pakundiona apukusa mutu.

26Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga:

Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu;

27kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu;

kuti Inu Yehova munachichita.

28 2Sam. 16.11-12 Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu;

pakuuka iwowa adzachita manyazi,

koma mtumiki wanu adzakondwera.

29 Mas. 35.26 Otsutsana nane avale manyazi,

nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.

30Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga;

ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.

31 Mas. 16.8; 121.5 Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi,

kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help