2 TIMOTEO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaPafupi mau onse opezeka mu Kalata yachiwiri ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Timoteo ndi malangizo opita kwa Timoteo yemweyo. Paulo akufuna kuti mnyamata wakeyo womthandiza pa ntchito yolalika, alimbikire pa udindo wake wochitira Yesu Khristu umboni, atsate mokhulupirika zophunzitsa zoona zopezeka mu Uthenga Wabwino ndiponso mu Chipangano Chakale. Asaleke kulalika ndi kuphunzitsa, ngakhale pakati pa mazunzo ndi zovuta zochokera kwa anthu ena. Azikana “mafunso opusa ndi opanda malango, podziwa kuti abala ndeu.” Koma ayesetse kutsata chitsanzo chomwe iye Paulo adapereka pa moyo wake wonse, pa za kukhulupirira, kuleza mtima, kukonda, kupirira ndi kulimbikira pa nthawi ya masautso.M'zonsezi, Paulo akukumbutsa Timoteo za m'mene iye mwini anakhalira ngati chitsanzo pa moyo wake ndi cholinga chake, chikhulupiriro chake, kupirira kwake, chikondi chake, ndi m'mene anazunzikira pa nthawi ya masautso.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Mau oyamika ndi olimbitsa mtima 1.3—2.13Malangizo ndi mau ena ochenjeza 2.14—4.5Atsate chitsanzo chomwe Paulo amusiyira 4.6-18Mau omaliza 4.19-22