1 Gen. 9.21; Yes. 28.7; Hos. 4.11 Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa;
wosochera nazo alibe nzeru.
2Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango;
womputa achimwira moyo wakewake.
3Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu;
koma zitsiru zonse zimangokangana.
4Waulesi salima chifukwa cha chisanu;
adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu.
5Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya;
koma munthu wozindikira adzatungapo.
6 Mat. 6.2; Luk. 18.11 Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake;
koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
7 Mas. 37.26; 1Maf. 15.4; 2Ako. 1.12 Wolungama woyenda mwangwiro,
anake adala pambuyo pake.
8Mfumu yokhala pa mpando woweruzira
ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.
9 1Maf. 8.46; Mas. 51.5; 1Yoh. 1.8 Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga,
ndayera opanda tchimo?
10 Deut. 25.13-15; Mik. 6.10-11 Miyeso yosiyana, ndi malichero osiyana,
zonse ziwirizi zinyansa Yehova.
11 Mat. 7.16, 20 Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake;
ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
12 Eks. 4.11 Khutu lakumva, ndi diso lopenya,
Yehova anapanga onse awiriwo.
13 Aro. 12.11 Usakonde tulo ungasauke;
phenyula maso, udzakhuta zakudya.
14Wogula ati, Chachabe chimenecho,
koma atachoka adzitama.
15Alipo golide ndi ngale zambiri;
koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali.
16Tenga malaya a woperekera mlendo chikole;
woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.
17Zakudya za chinyengo zikondweretsa munthu;
koma pambuyo pake m'kamwa mwake mudzadzala tinsangalabwi.
18 Luk. 14.31 Uphungu utsimikiza zolingalira,
ponya nkhondo utapanga upo.
19 Aro. 16.18 Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi;
usadudukire woyasama milomo yake.
20 Lev. 20.9; Mat. 15.4 Wotemberera atate wake ndi amake,
nyali yake idzazima mu mdima woti bii.
21 Hab. 2.6 Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake;
koma chitsiriziro chake sichidzadala.
22 2Sam. 16.12; Aro. 12.17, 19; 1Ate. 5.15 Usanene, Ndidzabwezera zoipa;
yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.
23 Miy. 20.10 Miyeso yosiyana inyansa Yehova,
ndi mulingo wonyenga suli wabwino.
24 Miy. 16.9 Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;
munthu tsono angazindikire bwanji njira yake?
25Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika,
kuli msampha kwa munthu,
ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.
26Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,
niyendetsapo njinga ya galeta.
27 1Ako. 2.11 Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova;
usanthula m'kati monse mwa mimba.
28Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu;
chifundo chichirikiza mpando wake.
29 Miy. 16.31 Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao;
kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.
30Mikwingwirima yopweteka ichotsa zoipa;
ndi mikwapulo ilowa m'kati mwa mimba.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.