1Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.
2Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.
3Korona wakunyada wa oledzera a Efuremu adzaponderezedwa;
4ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.
5Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ake otsala:
6ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.
7Miy. 20.1; Hos. 4.11Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.
8Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udyo, palibe malo okonzeka.
9Yer. 6.10Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nachotsedwa pamawere?
10Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.
111Ako. 14.21Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;
12amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.
13Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.
14Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a mu Yerusalemu.
15Amo. 2.4Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
16Gen. 49.24; Mas. 118.22; Mat. 21.42; Mac. 4.11; Aro. 9.33; Aef. 2.20chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
172Maf. 21.13; Yes. 28.15Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.
18Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi.
19Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake.
20Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi chofunda chachepa, sichingamfikire.
21Yos. 10.10, 12; 2Sam. 5.20Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.
22Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.
23Tcherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.
24Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?
25Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo?
26Pakuti Mulungu wake amlangiza bwino namphunzitsa.
27Pakuti sapuntha mawere ndi chopunthira chakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya galeta pachitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba chitowe ndi chibonga.
28Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera.
29Mas. 92.5; Yer. 32.19Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.