CHIVUMBULUTSO 19 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kupasula kwa Babiloni. Chimwemwe ndi mayamiko mu Mwamba

1 Chiv. 11.15; 12.10 Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;

2Deut. 32.43; Chiv. 16.7pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.

3Yes. 34.10Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.

4Chiv. 4.4Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kunena, Amen; Aleluya.

5Mas. 135.1Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.

6Ezk. 1.24; Chiv. 11.15, 17Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

72Ako. 11.2Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.

8Yes. 61.10; Ezk. 16.10, 13Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9Mat. 22.2-3; Luk. 14.15-16Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10Mac. 10.26; 14.14-15; 1Yoh. 5.10Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.

Khristu agonjetsa chilombo ndi mneneri wonyenga

11 Chiv. 3.14; 6.2 Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.

12Chiv. 2.17; 6.2Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.

13Yes. 63.2-3; Yoh. 1.1Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu.

14Chiv. 7.9Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu.

15Mas. 2.9; Yes. 11.4; Chiv. 14.19-20Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.

16Chiv. 17.14Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.

17 Ezk. 39.17-18, 20; Chiv. 19.21 Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu,

18Ezk. 39.17-18, 20kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang'ono ndi aakulu.

19 Chiv. 17.13-14 Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.

20Chiv. 13.11-15; 20.10Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:

21Chiv. 19.15, 17-18ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help