1 1Yoh. 1.9 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga;
ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
2 Aro. 3.20 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;
pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.
3Pakuti mdani alondola moyo wanga;
apondereza pansi moyo wanga;
andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
4Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;
mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga.
5 Mas. 77.5, 10-11 Ndikumbukira masiku a kale lomwe;
zija mudazichita ndilingirirapo;
ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.
6 Mas. 42.2; 88.9 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:
Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.
7Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.
Musandibisire nkhope yanu;
ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
8 Mas. 46.5; 90.14 Mundimvetse chifundo chanu mamawa;
popeza ndikhulupirira Inu:
Mundidziwitse njira ndiyendemo;
popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
9Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;
ndibisala mwa Inu.
10 Mas. 25.4-5 Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;
Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
11Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu;
mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.
12Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga,
ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;
pakuti ine ndine mtumiki wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.