1Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,
21Maf. 3.5Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.
31Maf. 9.25Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
4Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,
52Sam. 7.12-16pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.
6Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;
7Deut. 4.25-26; Yer. 7.13-14pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
8Yer. 22.8-9Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali ino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba ino?
9Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adatulutsa makolo ao m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, nailambira, naitumikira; chifukwa chake Yehova anawagwetsera choipa chonsechi.
Za midzi adaimanga Solomoni, ndi zombo zake(2Mbi. 8.1-2)10Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;
11popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu mizinda makumi awiri m'dziko la Galileya.
12Ndipo Hiramu anatuluka ku Tiro kukaona mizinda adampatsa Solomoniyo, koma siinamkomere.
13Nati, Mizinda ino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naitcha dzina lao, Dziko lachikole, kufikira lero lino.
14Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri.
15Ndipo chifukwa chake cha msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomoni ndi chimenechi; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido, ndi Gezere.
16Pakuti Farao mfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mzindamo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni.
17Ndipo Solomoni anamanganso Gezere, ndi Betehoroni wakunsi,
18ndi Baalati, ndi Tamara wa m'chipululu m'dziko muja,
19ndi mizinda yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi mizinda yosungamo magaleta ake, ndi mizinda yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga mu Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.
20Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israele,
21ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.
22Lev. 25.39-40Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang'anira magaleta ake ndi apakavalo ake.
23Amenewo anali akulu a akapitao oyang'anira ntchito ya Solomoni, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira ntchito aja.
241Maf. 3.1; 7.8Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.
25Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, paguwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira paguwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.
26Ndipo mfumu Solomoni anamanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere uli pafupi ndi Eloti, m'mphepete mwa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.
271Maf. 10.11Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.
28Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.