1 Yer. 31.37; Afi. 3.5 Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.
2Aro. 8.29Mulungu sanataye anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,
31Maf. 19.10, 14Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.
41Maf. 19.18Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu aamuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadire Baala.
5Aro. 9.27Choteronso nthawi yatsopano chilipo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.
6Agal. 5.4Koma ngati kuli ndi chisomo, sikulinso ndi ntchito ai; ndipo pakapanda kutero, chisomo sichikhalanso chisomo.
7Aro. 9.31Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeze; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;
8Yes. 29.10monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.
9Mas. 69.22-23Ndipo Davide akuti,
Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,
ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango;
10 Mas. 69.22-23 maso ao adetsedwe, kuti asapenye,
ndipo muweramitse msana wao masiku onse.
11 Mac. 18.6 Chifukwa chake ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao chipulumutso chinadza kwa anthu akunja, kudzachititsa iwo nsanje.
12Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?
Potsiriza Mulungu adzapulumutsa Israele13 Mac. 9.15 Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;
141Ako. 9.22kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.
15Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa?
16Num. 15.18-21Ndipo ngati zipatso zoyamba zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.
17Yer. 11.16; Aef. 2.12-13Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,
18usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.
19Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikalumikizidwe nao.
20Aro. 12.16Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
21pakuti ngati Mulungu sanaleke nthambi za mtundu wake, inde sadzakuleka iwe.
22Aheb. 3.6, 14Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.
232Ako. 3.16Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso.
24Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?
25 Luk. 21.24; Aro. 11.7 Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
26Yes. 59.20-21ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,
Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi;
Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:
27 Yes. 27.9 Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo,
pamene ndidzachotsa machimo ao.
28 Deut. 7.8 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.
29Num. 23.19Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.
30Aef. 2.2Pakuti monga inunso kale simunamvere Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,
31choteronso iwo sanamvere tsopano, kuti iwonso akalandire chifundo, chifukwa cha chifundo cha kwa inu.
32Agal. 3.22Pakuti Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akachitire onse chifundo.
Ulemu waukulu wa Mulungu33 Deut. 29.29; Mas. 36.6 Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
34Yes. 40.13Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala phungu wake ndani?
35Yob. 41.11Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso?
36Aef. 3.21; Akol. 1.16Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.