EZEKIELE 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Machimo oopsa a Yerusalemu

1Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2Nah. 3.1Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mzindawo wa mwazi kodi? Uudziwitse tsono zonyansa zake zonse.

3Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.

41Maf. 9.7; 2Maf. 21.16Wapalamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zakozako; chifukwa chake ndakuika ukhale chitonzo cha amitundu ndi choseketsa cha maiko onse.

5Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.

6Taona akalonga a Israele, yense monga mwa mphamvu yake, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.

7Eks. 22.21-22; Deut. 27.16Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.

8Lev. 19.30Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.

9Eks. 23.1Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.

10Lev. 18.7-8, 19; 1Ako. 5.1Anavula umaliseche wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anachepsa wodetsedwa ndi kooloka kwake.

11Lev. 18.9-20Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.

12Eks. 22.25; 23.8Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.

13Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.

14Ezk. 17.24Mtima wako udzaimika kodi, manja ako adzalimbikira masikuwo ndidzachita nawe? Ine Yehova ndanena, ndidzachichita.

15Deut. 4.27Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikuchokere.

16Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

17Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

18Yes. 1.21-22Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israele yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi chitsulo, ndi ntovu, m'kati mwa ng'anjo; ndiwo mphala zasiliva.

19Yes. 1.21-22Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, chifukwa chake taonani, ndidzakusonkhanitsani m'kati mwa Yerusalemu.

20Mala. 3.3Monga asonkhanitsa mtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi ntovu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzivukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.

21Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukuvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pake.

22Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwake; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.

23Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

24Wobadwa ndi munthu iwe, nena ndi Yuda, Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, losavumbwa mvula tsiku la ukalilo.

25Hos. 6.9Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.

26Mala. 2.7-8Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.

27Mik. 3.1-2Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.

28Ezk. 13.9-11Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova.

29Yer. 5.26-28Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.

30Yes. 59.16; Yer. 5.1; Ezk. 13.5Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.

31Ezk. 7.4; 22.22Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pamutu pao, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help